Cassim Ibrahim – Kumathokoza – Lyrics

0

VERSE 1
Waliona Tsiku Uziyamika Yehova,
Wakupatsa Ntchito Wakuchotsa Pa Ulova…
Uli Bwino Ena Akuvutika Ndi Matenda,
Ena Zinayima Koma Zako Zikuyenda…

Uli Ndi Ziwalo Zonse Ulibe Ulumali,
Wakufikitsa Apa Kukuchotsa Kutali…
Wakudalitsanso Iwe Ndi Banjali,
Madalitso Achuluka Ndi Ana pa Mbali…

Usakhale Ndi Nkhawa,
Kulingalira Za Mawa,
Chimwemwe Chidza M’mawa,
Likawala Dzuwa Moyo Uzafewa…

CHORUS
Kumathokoza…!
Ndi Wa Chikondi Chauta!
Kumayamika…!
Pa Zabwino Zomwe Amachita!

Kumathokoza…!
Watisunga Ndi Moyo Chauta!
Kumayamika…!
Pa Zabwino Zomwe Iye Wachita!

Mutamandeni Iye…!
Amen! Amen!
Aleluya…!
Amen! Amen!

Mutamandeni Iye…!
Amen! Amen!
Aleluya…!
Amen! Amen!

VERSE 2
Usakhale Ndi Moyo Womangodandaula,
Zifukwa Ndi Zambiri Zomuyamikira,
Yang’ana Komwe Iwe Wachokera,
Wakupyoletsa Muzambiri Wakusamalira…

Zomwe Ulinazo Ena Alibe…!
Anzako Unkacheza Nawo Ena Lero Kulibe…!

(Back to Chorus)

BRIDGE
Wakufikitsa Lero Ndi Chisomo Chabe…!
Ngakhale Umachimwa Wakusungabe…!
Uzikhala Ndi Nthawi Yokweza Dzina Lake…!
Poti Alinganiza Zonse Mu Nthawi Yake…!

(Back to Chorus… chorus repeats until it fades)

Leave a Reply

This website uses cookies to improve your experience. We'll assume you're ok with this, but you can opt-out if you wish. Accept Read More